Zathuzathu Sports Page

Zathuzathu Sports Page Sangalalani Ndi Zamasewero Zotyakuka Ndi Zathuzathu Sports Page
(1)

Today's results
20/06/2026

Today's results

Mphunzitsi watsopano wa FCB Nyasa Big Bullets, Edison Nyirenda, wauza akulu-akulu a timuyi  kuti agule osewera  anayi po...
19/06/2026

Mphunzitsi watsopano wa FCB Nyasa Big Bullets, Edison Nyirenda, wauza akulu-akulu a timuyi kuti agule osewera anayi pofuna kuonjezera mphamvu.

Nyirenda wati timuyi ikufunika otchinga kumbuyo awiri, osewera pakati komanso osewera kutsogolo.

Iye wayankhula izi dzulo pa msonkhano wa olemba nkhani pamene amafotoza m'mene akozekerera masewero awo ndi Kamuzu Barracks mu FDH Bank Premiership pa bwalo la Civo mu nzinda wa Lilongwe.

Bullets ilipanambala yachisanu ndi chimodzi ndimapointi khumi pamasewero asanu ndi chimodzi amene yasewera.

Ndalama zokwana K200 million ndi zomwe zikuyembekezeka kugwiritsidwa ntchito pokonzanso bwalo la zamasewero la Champions...
17/06/2026

Ndalama zokwana K200 million ndi zomwe zikuyembekezeka kugwiritsidwa ntchito pokonzanso bwalo la zamasewero la Champions ku Mponela m`boma la Dowa.

Mwini wake wa bwaloli King Msaiwale Kabvina, wati ntchito yokonza bwaloli ikuyembekezeka kuyamba posachedwapa ndipo pakadali pano ndalama zomwe zigwiritsidwe tchito zapezeka kale ndipo ntchitoyi idzafika kumapeto mchaka cha 2027.

Matimu a Kamuzu Barracks komanso Mafco FC, anasankha kuti bwalo la zamasewero la Champions kuti adzigwiritsa ntchito ngati pakhomo pawo m`masewero amumpikisano wa FDH Bank Premiership.

Mvula komanso mphepo ya mphavu inaononga denga la bwalori komanso malo ena okhalapo anthu Lowruka pa 6 June.

The Football Association of Malawi (FAM) has formally charged the Super League of Malawi (SULOM) with five disciplinary ...
16/06/2026

The Football Association of Malawi (FAM) has formally charged the Super League of Malawi (SULOM) with five disciplinary offences for deliberately defying a stadium safety directive.

SULOM scheduled a match at Kamuzu Stadium on April 25, just two days after FAM declared the venue unsafe pending inspection. Despite the explicit April 23 prohibition, SULOM publicly announced it would proceed regardless.

FAM accuses SULOM of failure to comply with statutes and directives, failure to prevent practices jeopardizing match integrity, "willful and deliberate disregard" of lawful FAM directives, and conduct bringing football into disrepute.

FAM's Disciplinary Committee will convene on Saturday, June 20, at Nkopola Lodge in Mangochi.

SULOM General Secretary Williams Banda confirmed receipt of the notice and said they will oblige.

16/06/2026

🚩 Today’s World Cup games:

🇫🇷 France - Senegal 🇸🇳 (21:00)
🇦🇷 Argentina - Algeria 🇩🇿 (03:00)
🇮🇶 Iraq - Norway 🇳🇴 (00:00)

Super League of Malawi (SULOM) has moved the FDH Bank Premiership match between Blue Eagles FC and Karonga United FC to ...
16/06/2026

Super League of Malawi (SULOM) has moved the FDH Bank Premiership match between Blue Eagles FC and Karonga United FC to Nankhaka Stadium from Aubrey Dimba Stadium.

The development follows the certification of Nankhaka Stadium to host elite football matches. The match is scheduled for Sunday, June 21.

SULOM has also rescheduled to Sunday from Saturday, the match involving Masters FC and Creck Sporting Club, due to the unavailability of the Bingu National Stadium on Saturday.

The FDH Bank Premiership is back⚽️🔥Here are the fixtures for week 7
15/06/2026

The FDH Bank Premiership is back⚽️🔥
Here are the fixtures for week 7

Timu ya Creck Sporting Club yalengeza kuti yalemba ntchito Ernest 'Livewire' Mtawali pa udindo wa mphunzitsi wamkulu wat...
11/06/2026

Timu ya Creck Sporting Club yalengeza kuti yalemba ntchito Ernest 'Livewire' Mtawali pa udindo wa mphunzitsi wamkulu watsopano wa timuyi.

A Mtawali, amenenso anaphunzitsapo timu ya Flames pakati pa zaka za 2015 ndi 2016, alowa mmalo mwa Eliyah Kananji amene timu ya Creck Sporting Club yawachotsa ntchito dzulo pamodzi ndi Harrison Saidi komanso Blessings Tembo.

Mlembi wamkulu wa Creck Sporting Club, Aaron Mtaya, wati a Mtawali, amene anasewera mu timu ya Flames kuyambira 1983 mpaka 2003, sanapatsidwe mulingo otenga chikho chilichonse, koma akudziwa kuti ntchito yawo yayikulu ikhale kupulumutsa timuyi kuti isatuluke mu ligi.

A Mtaya atinso a Mtawali apatsidwa ufulu osankha anthu amene adzigwira nawo ntchito limodzi.

Timu ya Creck Sporting Club, imene isewere nawo mu chikho cha Airtel Top 8, ili pa number 16 pa mndandanda wa ma timu a mu ligi ya FDH Bank Premiership ndi 2 points pa masewero asanu ndi imodzi amene yagonja anayi komanso kufananitsa mphamvu masewero awiri.

Timu ya FCB Nyasa Big Bullets yasankha a Wedson Nyirenda aku Zambia ngati mphunzitsi watsopano wa timuyi. A Nyirenda omw...
10/06/2026

Timu ya FCB Nyasa Big Bullets yasankha a Wedson Nyirenda aku Zambia ngati mphunzitsi watsopano wa timuyi.

A Nyirenda omwe anakhalako mphunzitsi wamkulu watimu ya masewero a mpira ku Zambia, awalandira pa msonkhano wa atolankhani ku Blantyre.

Mwamulandira bwanji Coach Maule ?

Woimbira masewero a mpira wa miyendo wadziko la Somalia, Omar Abdulkadir Artan, yemwe wakanizidwa kulowa mdziko la Ameri...
10/06/2026

Woimbira masewero a mpira wa miyendo wadziko la Somalia, Omar Abdulkadir Artan, yemwe wakanizidwa kulowa mdziko la America wafika ku Istanbul paulendo wake obwelera kwawo.

Artan wayamikira mabungwe a FIFA ndi Confederation of African Football kaamba ka mwai omwe anampasa.

Pakadali pano iye wakana kuyankhulapo zambiri pakukanizidwa kwake kulowa dziko la America kwa atolankhani omwe anamfunsa mafunso.

Mneneri wabungwe la FIFA wati Artan sangaloledwenso kuimbira masewero ena aliwonse kumpikisano wa World Cup wachaka chino (2026).

Artan ndi yemwe anasankhidwa kuti ndioimbira wabwino kwambiri muno mu Africa.

Address

Pretoria

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Zathuzathu Sports Page posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Share

Category