18/02/2023
MEETING OF ALL ZONES OF LILONGWE DISTRICT FOOTBALL COACHES ASSOCIATION AT LILONGWE COMMUNITY GROUND ON 18TH FEBRUARY, 2023
-Opening prayer by Likuni-Chinsapo Zone.
PRESENT
1. Nanthenje Zone
2. Mitundu Zone
3. Area 36 zone
4. Likuni-Chinsapo zone
5. Lilongwe District Coaches Committee
6. Kabudula Zone
7. Area 49 Zone
*AGENDAS:*
*1. Zomwe zachitika mma Zone mu chaka cha 2022:*
*Likuni-Chinsapo zone: Committee sili active and palibepo icho yachitapo.
*Mitundu Zone: Committee pachiyambi inali active koma pano yazilara.
*Area 36 Zone: Committe yawoso ndiyakufa.
*Mma Zone ambiri zikuonesa kuti mwakhala muli chetechete makamaka mu chaka cha 2022.
*LDCC chaka cha 2022 yayendera ma zone ngati: Nsalu, Chilinde, Area 49, Biwi, Mitundu, Likuni-Chinsapo, Kabudula.
*LDCC yinatsegula account ku FDH Bank ndicholinga choti kuti ikamapangisa ma course a Coaching anthu azitha kumaponya kumeneko ndalama yopangitsira course yo. Ndipo a Chairman atumiza account number yo pamaGroup onse amaZone a LDCC.
*2. Zomwe zichitike mcha cha 2023:*
-MaCoaches ambiri mmaZone akufunisisa kuti pachiyambi penipeni kuti ma Committee akhale active akuyenera a LDCC apangise mamphunziro a Coaches mma zone.
-Maganizo ena akuti mamphunziro a Coaches akuyenera kuchitika koma kwapanopa kwa ma Leaders a mma Zone kaye.
-Course ya FAM D License 🪪 yonse imakwana K3,000,000 pa anthu 30 koma paliso kuthekera kuonjezerekapo anthu.
-A Chairman a LDCC akhala pansi ndi a FAM kuwapempha kuti mamphunziro a Coaches achitike makamaka a FAM D LICENSE pa anthu ambiri and also pamtengo woti aliyense mkuthekera kupanga nawo ndipo alengeza posachedwapo zomwe iwo ayankhidwa or zomwe apeza. Pamene akhaleso akusaka sponsorship pa mamphunzirowa.
*AOB*
-A Chairman a LDCC ati pomatha chaka chino cha 2023 mamumphunziro a Coaching Course akhalapo ndithu.
-FAM chaka chino yatikonzera ma courses angapo makamaka pa Coaching License ya CAF C mu chaka chino cha 2023 kwa ma Coaches omwe ali ndi FAM D and FAM C License.
-MaDate ake ali motere: mu April kuli course ina, mu June-July kuliso course yina ndi mu September course ina pa mamphunziro Coaching License ya FAM C.
*Ndipo oyenera kukakhala nawo pa CAF C Coaching course iyi akhale mamembala wa Football Coaches Association of Malawi palilipira:
K7500 kwa iwo a FAM D and FAM C
K10000 kwa iwo ali ndi FAM B
K15000 kwa iwo ali ndi FAM A
-Closing prayer by Likuni-Chinsapo Zone