08/06/2026
DANGER WAPAKIRA KU TIMES WALOWERA KU JOJO FM
Williams Gondwa, yemwe amadziwika ndi dzina loti Danger Left Winger, wasintha nthabwa pomwe wachoka Times Radio mkuyamba ntchito ku JOJO FM malingana ndi zomwe yalemba wailesi ya Jojo mamawa uno pa tsamba lake la mchezo la Facebook.
“Tithandizeni kulandira katswiri oulutsa nkhani za masewero Williams Gondwa amene amadziwikanso kuti Danger Left Winger pamene wapanga join team ya nkhumekume zoulutsa mawu pa wayilesi ya JoJo 100.4 komanso 100.6 FM.”
_____________________________________________
🗣️🎙️ Open fayaaaaaaaaaaaaaaaaaaa! Kudzaphonya chikadakhala chigoli, mwayiiiiiiiii goalkeeper mbambande anasiya nthaka ndikumata Mpira ngati mmanja muli ulimbo... Mzanga Isaac Salimaaaa! Khuda Muyaba anazula buleti la mphamvu kwambiri bwezi tikukamba kuti ndi momujabe 0-0. 🙌😅
🗣️🎙️ Yes, referee waliza pinto yake Akuti panali ngati kukankhana-kankhana ndiye ndi Mpira wapansi. Kudzangowutsetseletsa wamphamvu kwambiri ngati madzi ayamba mafunde pa Nyanja, apite Emmanuel Savieli kubwiza njomba yoyamba yachiwiri mkudzatheka, kudzakokotela-kokotela kumene kuja koma Peter Cholopi waima njiii ngati chitsa chotsala mulupsya 🙌😅
🗣️🎙️ YEEESSSSSS, grade 1 referee Godfrey Nkhakananga waliza pinto, kuti chigawo chachiwiri chathela pomwepo. Osaonetsa kutopa komanso osafowoka, Williams Gondwa, Danger Left Winger wapitaaaa!
— ADD YOURS 👇😸