18/09/2023
NKHANI ZAMAPHELEPHELE
♦️ Timu ya Aston Villa ili ndi malingaliro ofuna kudzagula katswiri otseka kumbuyo kwa timu ya Real Sociedad, Robin Le Normand mu January.
♦️ Mphunzitsi wa timu ya Getafe wanena k*ti, Jude Bellingham ndiyemwe ananyengerera Mason Greenwood ak*ti ayambe kusewerera matimu aku Spain.
♦️ Timu ya Arsenal yatsala pang'ono kumalizitsa chili chonse k*ti mtsogoleri wa osewera wawo, Martin Odegaard anjozere mgwirizano wa tsopano ndi timuyi.
♦️ Timu ya Barcelona ili ndi malingaliro ofuna kudzagula katswiri omwetsa zigoli ku timu ya Newcastle United, Alexander Isak k*ti adzakhale mlowammalo wa osewera wawo Robert Lewandowski yemwe ali ndi zaka 35.
♦️ Timu ya Newcastle United yadyerera maso pa katswiri wa timu ya West Ham, Lucas Paqueta, ndipo Newcastle ndiyokonzeka kulipira ndalama zokwana 52 million pounds.
♦️ Matimu a Manchester United, Arsenal komanso Liverpool ndiwokonzekeka kulimbirana katswiri wapakati wa timu ya FC Salzburg, Oscar Gloukh.
♦️ Timu ya PSG inapanga chiganizo chosafuna kugula Jude Bellingham kuchoka ku timu ya Borussia Dortmund chaka chatha.
♦️ David Moyes wayamikira katswiri wakale wa timu ya Manchester United, Jesse Lingard kamba ka mmene akuchitira bwino ku training. Lingard wakhala akupanga zokonzekera limodzi ndi timu ya West Ham kwa masabata angapo tsopano.
♦️ Timu ya Manchester City ikunyalanyaza kuyamba zokambirana ndi katswiri wawo wapakati, Kelvin Dr Bruyne k*ti aonjezere mgwirizano wake k*timuyi. De Bruyne watsala ndi miyezi 18 yokha k*ti mgwirizano wake ndi timu ya Manchester City uthe.
♦️ President Wa timu ya Aston Villa wadyerera zintchito za katswiri WA timu ya Athletic Bilbao, Nico Williams.
♦️ Ngakhale Joao Palhinha waonjezera mgwirizano wake ku timu ya Fulham, timu ya Bayern Munich sikugona tu