29/05/2026
Katswiri wakale wa team ya Mighty Wanderers FC Lawrence Chaziya yemwe pakadali pano akutumikira team ya Simba Bhola mdziko la Zimbabwe Ali pa mndandanda wa Osewera 8 omwe sapezeka nawo mmasewero akubwelawa.
Lawrence Chaziya ali ndima Yellow card awiri ndipo iye pamalamulo sakuyenera kupezeka mmasewero amodzi amu league, timu ya Simba Bhola FC yomwe ili pa number 8 ndi mapointi 20 pamasewero 14 amu league ndipo ikhale ikukumana ndi team ya Triangle FC yomwe ili pa number 17 ndipo ili ndi 8 points pamasewero 14 yomwe nayo yasewera.
Chaziya wakhala osewera odalilika ku team ya Simba Bhola FC season ino ndipo masabata apitawo a apezeka nawo mu team of the week ya mdzikolo pamodzi ndi Binwell Katinji yemwe akutumikira team ya Chicken Inn.
✍️ Obanda 50
DRYBORNE SPORT