06/07/2026
🚨 Karonga United yalengeza kuti wayimitsa pa ntchito mphunzitsi wao wamkulu Audrow Makonyola kwa masewero atatu kutsatira kusachita bwino kwa timuyi mu ligi ya FDH pomwe angokwanitsa kupambana kawiri, kugonja kanayi ndi kufananitsa mphamvu katatu m'masewero 9.
Timuyi yomwe ili pa nambala 13 pakadali pano inagonja 3-1 ndi timu ya GC Dedza Dynamos m'masewero aposachedwa.
Chris Crespo Chinkwita ndi yemwe wapatsidwa ntchito yogwirizira.
Wolemba : Jamie Michael
GBS TV sports desk