29/03/2026
Super League of Malawi (Sulom) yatulutsa ndondomeko ya masewero a season ya 2026/2027 kuyambira loweruka pa 25 April, 2026 mpaka pa 20 February, 2027.
Tsiku lotsegulira, akatswiri Mighty Wanderers adzayambira ndi masewero apa khomo pa Kamuzu mu nzinda wa Blantyre ndi Karonga United, pamene FCB Nyasa Big Bullets iyamba ndikoyenda pamene idzasewera ndi
Civil Service United pa bwalo la Civo ku Lilongwe, ndipo
Kamuzu Barracks idzaitanitsa Silver Strikers pa bwalo la Champions ku Dowa, pamene Moyale Barracks idzaswana ndi Goshen City Dedza Dynamos pa pa bwalo la Mzuzu.
Ndipo pa tsiku lotsatira, lamulungu pa 26 April 2026 timu ya Blue Eagles FC idzakumana ndi Ekhaya FC pa bwalo la Nankhaka mu nzinda wa Lilongwe, pamene Red Lions idzakumana ndi Creck Sporting Club pa bwalo la Balaka, ndipo Mafco FC idzathana ndi timu ya Mitundu Baptist pa bwalo la Champions ku Dowa, pamene Masters Security FC idzaitanitsa Chitipa United pa bwalo la Civo mu nzinda wa Lilongwe.
Mlembi wa Sulom yemwenso ndi mkulu wa komiti yoona ndondomekoyi, Williams Banda, wauza atolankhani lero mu nzinda wa Blantyre kuti ndondomekoyi yatulusidwa mogwirizana ndi kalendala ya Football Association of Malawi (FAM).
Banda wati salola kuti matimu azipempha masewero oyenera kukumana nawo kamba koti izi zimasokoneza.
Iye waonjezera kuti timu ina iliyonse ikuyembekezereka kusewera pafupi-fupi masewero asanu ndi awiri pa khomo, likamatha gawo loyamba ndipo ena adzasewera gawo lachiwiri.
# football season is back π₯π₯π₯