05/10/2023
"PHADA AMENEYO SINDIVINA NAWO" - GONDWE
M'modzi mwa akulu-akulu a timu ya Mighty Mukuru Wanderers FC, Chancy Gondwe waulula kuti sapanga appeal chigamulo chake ku komiti yaikulu ya bungwe la Football Association of Malawi ndipo m'malo mwake akamang'ala kubwalo lalikulu la milandu la High Court.
Gondwe walankhula izi poyankhapo pa chilango chimene Iye walandira kudzera ku komiti yosungitsa mwambo kubungwe la FAM potsatira kumupeza olakwa pazomwe anauza tsamba lina lolemba nkhani zamasewero kunena kuti akulu-akulu a mu komiti yosungitsa mwambo anapereka chilango kutimu yake cholipira ndalama zokwana K24.5 million kukhala ngati kuti analedzera.
Kudzera mu chikalata chimene bungwe la FAM latulutsa Lachiwiri, bungweli lalamula Gondwe, amene ndi Mlangizi wa zamalamulo kutimu ya Wanderers, kuti alipire K1.2 million pa milandu itatu imene anamupeza nayo kuti ndiolakwa yomwe ndi kunyazitsa masewero a mpira wamiyendo, kunyazitsa akulu-akulu a bungwe la FAM komanso kuononga dzina la kampani ya Airtel imene ndi mthandizi wa chikho cha Airtel Top 8.
Mukalatayi, FAM linapereka maola okwana 72 kwa Gondwe kuti apange appeal chigamulochi ku komiti yaikulu yosungitsa mwambo kubungwe-li ngati sakukhutira nacho.
Koma polankhula ndi wayilesi ya Times, Gondwe wati alibe nthawi yopanga appeal chigamulochi kubungwe la FAM ndipo m'malo mwake Iye akamang'ala ku bwalo lalikulu la High Court.