02/09/2025
Babatunde sopano ndi Malawi
Osewera wa ku sogolo wa timu ya Fcb Nyasa Big Bullets Babatunde sopano ndi fulu mu dziko lino la Malawi.
Babatunde sopano walandila chiphaso cha uzika ndipo atha kupanga chilichonse ngati mzika ya Malawi kuphatikiza kutumikila timu ya dziko lino.
Babatunde atha kupezeka mu gulu la osewera omwe atenge mbali pa masewero awiri omwe timu yathu ya dziko lino isewere mwezi uno.
Pali chiyembekezo choti Pasuwa ayitana osewerayu kamba koti ndi amene akusogola zigoli mu league ya dziko lino komaso ndi ovomerezeka kusewera timu yathu ya dziko lino.