04/05/2023
Timu ya Silver Strikers kudzera kwa ma loya ake, yapereka umboni ku bungwe la FAM, owonetsa kuti Hassan Kajoke analandira 3 million Kwacha ngati chipondamthengo (signing-on fee) komanso malipiro a miyezi iwiri (450,000 Kwacha) miyezi ya January ndi February.
Bungwe la FAM linalembera timuyi kuti itulutse umboni oti Kajoke anasayina mgwirizano wa zaka zitatu ndi timuyi, kuyambira pa 04 January, 2023 mpaka 03 January, 2026 ndipo analandira kale ndalama za mgwirizanowu.
Mu kalata yawo, ya pa 28 April, 2023, ma loya a timuyi ati sakukhutira ndi mmene bungwe la FAM likuyendetsera nkhaniyi chifukwa osewerayu samayenera kuloledwa kuseweranso mpira kufikira nkhaniyi ithe mwa chilungamo komanso motsata malamulo.
Timu ya Silver, kudzera kwa ma loyawa, yati ndi yodabwa kuti Kajoke anasewera nawo masewero a ligi amene timu ya FCB Nyasa Big Bullets inasewera ndi Extreme FC pa 29th April, 2023 ku Lilongwe.
Timu ya Silver inakasuma ku bungwe la FAM kuti lipatse Kajoke chilango chosaseweranso mpira kamba ka ukamberembere ndi chinyengo pamene anasayinanso mgwirizano wa zaka zitatu ndi timu ya Nyasa Big Bullets chonsecho anasayina kale mgwirizano wina ndi timu ya Silver.
......✍️✍️