26/11/2025
Super League of Malawi (Sulom) yavomera kuti yalandira kalata ya madandaulo yomwe Mighty Wanderers yawalembera yokhudza masewero ndi timu ya Silver Strikers.
Wanderers inadandaula kuti oyimbira pamasewerowa, Samuel Fudzulani, anawakanira chigoli chomwe osewera wawo, Clement Nyondo, anagoletsa zomwe kwaiwo akuti panalibe offside ili yonse.
Manoma apemphanso kuti masewerowa awunikidwe ndikuwapatsa mapointi onse atatu kamba koti pachilungamo iwo ndi amene anapambana ngakhale anathera kufanana mphamvu pogoletsana zigoli ziwiri kwa ziwiri.
Timu yaku Lali Luban yatinso oyimbirayu apatsidwe chilango komanso asadzaimbire masewero ali onse a timuyi.
Koma poyankhapo, wachiwiri kwa mlembi wa Sulom, Donnex Chilonga, wati akhala pansi ndikuunika zomwe Manoma adandaula ngati zili zoona kapena ayi kudzera ku National Football Referees Association (NFRA).
Chilonga watinso asanapange ganizo pa nkhaniyi akagogoda khomo la komiti ya oyimbira ku Football Association of Malawi (FAM) ndicholinga choti nawonso ayikepo mlomo pa nkhaniyi.
Manoma ali panambala yachiwiri mu TNM Super League ndimapointi 52 pamasewero 22, pamene FCB Nyasa Big Bullets ndiyomwe ikutsogola ndi mapointi 53 pamasewero 23.